QUR’AN YOLEMEKEZEKA yotanthauzidwa m’chichewa
Pamene ndimagwira ntchitoyi, panali mabuku amene ndimathandizika nawo pakasankhidwe ka kutanthauzira koyenera kwa Qur’an, komanso anthu amene amandithandiza pakasankhidwe ka mawu oyenera m’chichewa. Mabukuwa ndi awa Tafsiri ya Jalalain, Tafsiri ya ibn Kathiri, Al Muntakhab ndi Swafuat Tafaasiri. Ndipo Ntchito yotanthauzira inatha m’chaka cha 1987 pambuyo poigwira mzaka zitatu. Ndipo kuyambira nthawiyo kufikana m’chaka cha 1999 yakhala ikuunikidwa ndi ma Sheikh akuluakulu m’dziko muno.









