
SWAUM(KUSALA) ILI MMAGULU AWIRI
الزكاة CHICHEWA اللغة العربية ZAKATI ILI MMAGULU AWIRI الـزكاة قـسـمان: YA SUNNAH: Ndipo ichi ndi chuma chilichonse chimene munthu amapeleka mu njira ya ibadah(kumpembedza Mulungu). نافلة : و هي كل مال يخرجه الإنسان على وجه التعبد المحض . YA FARADH (YOKAKAMIZIKA) فريضة : Iyi ili mmagulu awiri: 🙁 وهي نوعان ) ZAKATI YA ZAKUDYA: Iyi ndi imene imatchedwa kuti Zakatul fitir, imene imapelekedwa ku mapeto...
SWAUM(KUSALA) ILI MMAGULU AWIRI
الزكاة
CHICHEWA | اللغة العربية |
ZAKATI ILI MMAGULU AWIRI | الـزكاة قـسـمان: |
YA SUNNAH:
Ndipo ichi ndi chuma chilichonse chimene munthu amapeleka mu njira ya ibadah(kumpembedza Mulungu). |
نافلة :
و هي كل مال يخرجه الإنسان على وجه التعبد المحض . |
YA FARADH (YOKAKAMIZIKA) | فريضة : |
Iyi ili mmagulu awiri: | 🙁 وهي نوعان ) |
ZAKATI YA ZAKUDYA:
Iyi ndi imene imatchedwa kuti Zakatul fitir, imene imapelekedwa ku mapeto kwa mwezi wa Ramadhani, ndipo ndiyokakamizika kwa msilamu aliyense, wamkulu,wamng'ono, wammuna kapena wamkazi,kapolo kapena mfulu. |
زكاة بدن :
وهي زكاة الفطر. وهي واجبة على كل مسلم: كبير أو صغير, ذكر أو أنثى, عبد أو حر . |
ZAKATI YA CHUMA(NDALAMA):
Tanthauzo lake pa sharia:uku ndi kumpembedza Allah popeleka gawo lomwe lili lokakamizika pa sharia kuchokera mu chuma chodziwika bwino,chumacho chipite ku kagulu kapena mbali yodziwika bwino. Ndipo imeneyi ndi msichi yachitatu mu msichi za chisilamu. Zakati imeneyi ili mmagulu anayi(4). |
زكاة مال :
حدها شرعاً 🙁 التعبد لله تعالى بإخراج جزء واجب شرعاً في مال معين لطائفة أو جهة مخصوصة) وهي الركن الثالث من أركان الإسلام, وتنقسم إلى أربعة أقسام : |
1-NDALAMA ZIWIRI:
Golide ndi Siliva kumpatikizaponso mtundu ulionse wa ndalama (ngati ma kwacha). Golide mulingo wake ndi 20(omwe ndi ma galamuzi 85). Pomwe mulingo wa Siliva ndi 200( omwe ndi ma galamuzi okwana 595). |
1 – النقدين :
الذهب والفضة وما يقوم مقامهما من عملات و غيرها, فنصاب الذهب 20 مثقالاً (85ج) ونصاب الفضة 200 درهم (595ج)
|
1- ZIWETO:
Zimene gawo lalikulu pa chaka zimadyetsedya ndi msipu waulele. Ndipo ziweto zake ndi monga: Ngamila, Ng'ombe, Mbuzi kapena Nkhosa. |
2- السّائمة :
التي ترعى المباح أكثر الحول أو كله والمقصود ببهيمة الأنعام: الإبل, والبقر, والغنم. |
3-ZOTULUKA MU NTHAKA:
Izi ndi Njere (monga chimanga) Ndi Zipatso (monga tende). |
3- الخارج من
الأرض : و هو الحبوب والثمار
|
4 -CHUMA CHA MALONDA:
Ichi ndi chilichonse chimene chaikidwa pa mndandanda wa kugula ndi kugulitsa(bizinesi). |
4 - عروض التجارة :
وهي كل ما أعد للبيع والشــراء |
ENI ZAKATI(OYENERA KULANDILA): | أهل الزكاة : |
OVUTIKITSITSA(MA FUQARAU):
Awa ndi ovutika omwe sapeza kalikonse, kapena amapeza zowakwanira zochepa kwambiri pa moyo wawo. |
الفقراء:
وهم أهل الحاجة الذين لا يجدون شيئاً, أو يجدون بعض الكفاية. |
OSAUKA(MISIKINI):
Awa ndi omwe amapezako zowathandiza zochulukilapo kapena theka pa Chaka. Titati tiyelekeze kuti ndalama imene ingakwanire kudya pa chaka ndi K12000. Ovutika aja ndiye kuti akhala ndi K6000, kapena alibiletu. Pomwe osaukawa ndiye kuti akhala ali ndi K6000 kapena kuposela pamenepo,koma safika pa K12000. Choncho ife timayenera kumpatsa ovutika ndi osauka yu chimene chingawakwanire pa chaka. Zili choncho chifukwa zakati imakakamizidwa chaka chikazungulila. |
المساكين:
وهم يجدون أكثر الكفاية أو نصفها, فلو قدرنا الكفاية لسنة مثلا بـ 12000 فالفقير هنا لديه ستة آلاف أو لا شيء. والمسكين من لديه ستة آلاف أو أكثر ولم يبلغ 12000, لاننا نعطي المسكين والفقير ما يكفيهما لسنة لأن الزكاة تجب في الحول . |
OGWIRA NTCHITO YA ZAKATI:
Awa ndi omwe amatolera,kusunga ndi kugawa zakati. Ntchito imeneyi amapatsidwa ndi mtsogoleli. Awa amapasidwa zakati osayang'ana kuti ndi osauka kapena olemela.ngakhale ali olemela amayenerabe kuti apatsidwe zakah. |
العاملون على الزكاة :
وهم جباتها وحفاظها والموكلون بقسمتها, يوليهم ولي الأمر ولا يشترط فيهم وصف الفقر, بل يعطون منها ولو كانو أغنياء
|
OFEWETSEDWA MITIMA YAYO:
Awa ndi omwe timayembekezera kuti atha kulowa chisilamu, kapena kusiya kwavutitsa asilamu(ngati atsogoleli adera) kapena omwe tikufuna kuwalimbikitsa chikhulupiliro chawo(imaan). |
المؤلفة قلوبهم :
ممن يرجى إسلامه أو كف شره أو قوة إيمانه
|
AKAPOLO:
Awa ndi: A- Msilamu yemwe walembeledwa kuti ngati atapeleka ndalama mwakuti basi amasulidwa ukapolo. B- Kummasula ukapolo msilamu. C- Msilamu yemwe wagwidwa ukapolo ku nkhondo. |
في الرقاب :
وهم : أ - المكاتب المسلم ب - إعتاق الرقيق المسلم ج - الأسير المسلم
|
OTHINIDWA NDI NGONGOLE:
Awa ndi: A- Yemwe wagwa mu ngongole chifukwa chofuna kuyanjanitsa anthu omwe asemphana. B- Yemwe wagwa mu ngongole chifukwa chofuna kuzithandiza pa mavuto ake omwe anamugwera. |
الغارمون :
وهم : أ- غارم لإصلاح ذات البين ب- غارم لنفسه
|
YEMWE ALI PA NJIRA YA ALLAH:
Umu mukulowa asilikali a nkhondo ndi kalikonse kamene angasaukile monga zida ndi zina zotero.
|
في سبيل الله :
يشمل الغزاة ومايحتاجون إليه من سلاح وغيره
|
WA PAULENDO:
Uyu ndi munthu yemwe wauyamba ulendo ndipo kamba wake wa pa ulendo watha (monga tarasipoti), choncho amapasidwa zokamufikisa kwawo komwe wachokera kapena komwe akulowera. |
ابن السبيل :
وهو المسافر المجتاز الذي قد فرغت نفقته, فيعطى ما يوصله إلى بلده
|

SWAUM(KUSALA) ILI MMAGULU AWIRI
Scan QR Code | Use a QR Code Scanner to fast download directly to your mobile device

( وماهو على الغيب بضنين ) viņš nav skops attiecībā uz atklāsmi, nedz arī slinko vēstījuma nodošanā un mācīšanā, bet gan sniedz visas zināšanas, kuras cilvēks ir gatavs saņemt, atšķirībā no zīlniekiem." Zīlnieki neko nedod, nemāca un nesniedz zināšanas, kuras apgalvo zinām, izņemot par samaksu.
April 22, 2025