IFE NDI NDANI?

Spread the love

من نحن ؟
IFE NDI NDANI?
اللغة التشيشيوا CHICHEWA

Ife ndi asilamu,
timmampembedza Allah M'modzi yekha,popanda kumphatikiza ndi aliyense,ndipo timatsatira Quran yolemekezeka ndi chiphunzitso cha Mtumiki Muhammad (mtendere ndi madalitso apite kwa iye) potengera kamvedwe ka maswahaba Allah asangalale nawo.

Chisilamu ndi chipembedzo cha umodzi wa Allah , chimaitanira zompembedza Allah yekha, kuchitirana chifundo,chilungamo ndi kukhala ndi chikhalidwe chabwino.

Ife timakhulupilira zoti ndithudi:
•Allah ndi M'modzi alibe ophatikizana naye.
•Quran ndi mawu a Allah.
•Muhammad (mtendere ndi madalitso apite kwa iye) ndi Mtumiki omaliza.
•Timakhulupilira za atumiki onse, monga Ibrahim, Mussah,Issah(Yesu) mwana wa Mariam, ndipo ife onsewo timakonda, komanso timakhulupilira za uthenga wawo.
•Timakhulupiliranso zoti kuli kuukitsidwa kwa akufa, kuwerengeseredwa zintchito zathu, Janna ndi moto.

Cholinga chathu ndiko kumpembedza Allah ndi kupindulitsa community.
System yathu ndi kuchita zinthu mwa pakati kati.

Timaitanira ku makhalidwe abwino, chifundo, chilungamo ndi kukhala bwino ndi anthu ena pa community.

Ndipo timakaniratu zopsyola malire ,mtopola ndi kuukila.

Timalemekeza malamulo ndi ndondomeko za dziko limene ife timakhalamo, ndipo timayesetsa ndi kufunitsitsa titakhala anthu abwino opindulira community yathu.

——
Mzikiti:

Mizikiti ndi malo amene ali oyera pa dziko lapansi, komanso omwe ali abwino kwambiri, ndipo izi ndi nyumba zomwe zinamangidwa ndi cholinga chompembedza Allah yekha basi.

Mzikiti si malo awina wake ayi, palibe yemwe ali ndi umwini pa mzikiti, koma mizikiti mwini wake ndi Allah basi. Ndi otsekugulidwa kwa aliyense amene akufuna kupanga mapemphero kapena kuphunzira za chisilamu, kapena kubwelera kwa Allah.

Zimatisangalatsa ife kulandila mafunso anu mwa ulemu onse komanso modekha.

——

Kodi ndi zotheka kwa yemwe sali msilamu kulowa nawo mu mzikiti?

Eya muli olandilidwa kuti mudzadziwe zambiri zokhuzana ndi chisilamu.

Ndizotheka kwa inu kupita ku mzikiti nthawi iliyonse yomwe ogwira ntchito akupezeka kapena aliyense opanga dawa yemwe ali ndi udindo olandila anthu ku mzikitiko, makamaka kwambiri:
•Nthawi yopemphera.
•Masiku awiri awa, Saturday ndi Sunday.
•Pa Eid Al-Fitir ndi Eid Al-Adhuha.
•Mu Ramadhan pamene anthu akumasula kusala kudya.

Mzikiti ndi malo opangira mapemphero, ophunzilira komanso ndi malo amtendere.

——
Zoyenera kutsatira pamene tikukazonda mzikiti:

•Kukhala ndi manyazi komanso ulemu, chifukwa imeneyo ndi nyumba imodzi mu nyumba za Allah.
•Kuvula nsapato tisanalowe malo opemphelera.
•Pali khomo komanso malo omwe anaikidwa kuti ndi opemphelera azimayi okha.

——

Ngati mutafuna kudziwa zambiri zokhuzana ndi chisilamu kapena kupempha buku la Quran:

https://sahaan.com/

Muli olandilidwa ku mzikiti.

Shopping Basket