MAPEMPHERO A HAJJI مناسك الحج

MAPEMPHERO A HAJJI
Kuvala ihram /kuiyamba Hajj.
Kupanga niyah yolowera mu mapemphero a hajji.
Malo opangira Niya kapena kuvalira ihram kwa anthu ochokera ku Shami ndi Egypt amatchedwa: al-Juhfah.ali pa mtunda otalika 186 kilometers kukafika ku Makkah.
Anthu ochokera ku Madinah malo awo ndi otchedwa al-Dhul-Hulayfah, mtunda otalika 420 kilometers.
Anthu ochokera ku Iraqi malo awo ndi otchedwa Dhatu-Iraq pa mtundu otalika 98 kilometers.
Anthu ochokera ku dera la Najid, malo awo ndi otchedwa Qarin al-Manāzil, mtunda otalika 99 kilometers.
Anthu ochokera ku Yemen malo awo ndi otchedwa Yalamulam, mtunda otalika 99 kilometers.
Anthu omwe akubwera pa ndege malo awo opangira ihram adzakhala olunjika ndi malo omwe ali pafupi ndi iwowo mu mlenga lengamo potengera malo atchulidwa aja.
Twawaf ya yemwe wafika kumene ku Makkah.
Udzayenda molunjika zizindikiro ziwiri za green, pambuyo pake udzathamanga kwambiri pakati pa zizindikiro ziwiri zimenezo, ndipo kuthamangaku eni ake ndi amuna okha basi.
Kuzukuzungulira ma round asanu ndi awiri (7), kuyambila pamene pali mwala wakuda kukafikanso pa mwala wakudawo.
POYAMBILA - POTHERA
Kuthamanga pakati pa Phiri la al-Aswafā ndi al-Mariwā
al-Aswafā - al-Mariwā
Usiku wapa 9 dhul-Hijjah
Kukagona ku MINA
Kuswali ku MINA ko swalah ya Dhuhur, Asir, Maghreb,ndi Eishah usana wapa 8 , kuswali Fajir tsiku lapa 9.
Pa 9 dhul-Hijjah
Kukaima pa Phiri la ARAFAT.
Kuimaku kumayambira pambuyo pa swala ya Dhuhur tsiku lapa 9,kulekezera pa swala ya Fajir tsiku lapa 10.

 

Adzaswali kumeneku swalah ya Dhuhur ndi Asir mophatikiza mopungula ma rakah komanso kuifulumizitsa Asir.

Usiku wapa 10:
Kukagona ku MUZIDALIFAT.
Uku adzaswaliko Maghreb ndi Eishah mophatikiza tsiku lapa 9, ndipo adzaswaliko Fajir tsiku lapa 10.
Pa 10 dhul-Hijjah:
Ugenda chipilala chotchedwa Jamaratul-Uqbah ndi timiyala tokwana tisanu ndi tiwiri (7).
Kupha chinyama kwa amene akupanga Hajj ya Tamatuu kapena Qarin.
Kumeta mpala kapena kuyepula tsitsi.
Mpala kapena kuyepula tsitsi izi ndi za amuna okha okha,pomwe akazi adzayepula tsitsi lawo pa mulingo wa nsonga ya chala ataliphatikiza pamodzi.
Twawaf yosunthira/kuchoka

(kusuntha kuchokera ku Arafat pambuyo poima)

Kukathamanga pakati pa Phiri la al-Aswafā ndi al-Mariwā kwa yemwe akupanga Hajj ya Tamatuu , kapena amene sanakathamange pambuyo pomaliza kuzungulira Kaaba (Twawaf) atangofika kumene.
kukagenda zipilala kenako kukagona ku MINA:
Pa 11,12, ndi 13 kwa omwe anachedwa kukagendako.
Kugenda zipilalaku kuyambira chipilala chaching'ono, kenako chapakatikati, kenako chachikulu, pambuyo pakupendeka dzuwa ( yomwe ili nthawi ya Dhuhur).
Chipilala:1
Chipilala:2
Chipilala:3
Malo opangira Duwa (pempho).
Twawaf yotsazikana ndi Makkah.
Imagwa kwa mzimayi amene wayamba matenda akumwezi (period), kapena matenda akubeleka(nifas).
Nsichi za Hajj:

Amene wasiya nsichi ingakhale imodzi yokha, ameneyo Hajj yake imakhala yosakwanira pokha pokha ataipanga nsichiyo.

zomwe zili wajib pa Hajj:

Yemwe wasiya cha wajib adzabwezeretsa pozinga chinyama.

Shopping Basket