| 1- ZIWETO:
Zimene gawo lalikulu pa chaka zimadyetsedya ndi msipu waulele.
Ndipo ziweto zake ndi monga: Ngamila, Ng’ombe, Mbuzi kapena Nkhosa. |
2- السّائمة :
التي ترعى المباح أكثر الحول
أو كله والمقصود ببهيمة الأنعام:
الإبل, والبقر, والغنم. |
| 3-ZOTULUKA MU NTHAKA:
Izi ndi Njere (monga chimanga)
Ndi Zipatso (monga tende). |
3- الخارج من
الأرض :
و هو الحبوب
والثمار
|
| 4 -CHUMA CHA MALONDA:
Ichi ndi chilichonse chimene chaikidwa pa mndandanda wa kugula ndi kugulitsa(bizinesi). |
4 – عروض التجارة :
وهي كل ما
أعد للبيع
والشــراء |
| ENI ZAKATI(OYENERA KULANDILA): |
أهل الزكاة : |
| OVUTIKITSITSA(MA FUQARAU):
Awa ndi ovutika omwe sapeza kalikonse, kapena amapeza zowakwanira zochepa kwambiri pa moyo wawo. |
الفقراء:
وهم أهل الحاجة الذين لا يجدون شيئاً,
أو يجدون بعض الكفاية. |
| OSAUKA(MISIKINI):
Awa ndi omwe amapezako zowathandiza zochulukilapo kapena theka pa Chaka.
Titati tiyelekeze kuti ndalama imene ingakwanire kudya pa chaka ndi K12000.
Ovutika aja ndiye kuti akhala ndi K6000, kapena alibiletu.
Pomwe osaukawa ndiye kuti akhala ali ndi K6000 kapena kuposela pamenepo,koma safika pa K12000.
Choncho ife timayenera kumpatsa ovutika ndi osauka yu chimene chingawakwanire pa chaka.
Zili choncho chifukwa zakati imakakamizidwa chaka chikazungulila. |
المساكين:
وهم يجدون أكثر الكفاية أو
نصفها, فلو قدرنا الكفاية لسنة
مثلا بـ 12000 فالفقير هنا لديه
ستة آلاف أو لا شيء.
والمسكين من لديه ستة آلاف
أو أكثر ولم يبلغ 12000, لاننا
نعطي المسكين والفقير ما
يكفيهما لسنة لأن الزكاة تجب
في الحول . |
| OGWIRA NTCHITO YA ZAKATI:
Awa ndi omwe amatolera,kusunga ndi kugawa zakati.
Ntchito imeneyi amapatsidwa ndi mtsogoleli.
Awa amapasidwa zakati osayang’ana kuti ndi osauka kapena olemela.ngakhale ali olemela amayenerabe kuti apatsidwe zakah. |
العاملون على الزكاة :
وهم جباتها وحفاظها والموكلون
بقسمتها, يوليهم ولي الأمر ولا يشترط
فيهم وصف الفقر, بل يعطون منها
ولو كانو أغنياء
|
| OFEWETSEDWA MITIMA YAYO:
Awa ndi omwe timayembekezera kuti atha kulowa chisilamu, kapena kusiya kwavutitsa asilamu(ngati atsogoleli adera) kapena omwe tikufuna kuwalimbikitsa chikhulupiliro chawo(imaan). |
المؤلفة قلوبهم :
ممن يرجى إسلامه أو كف شره أو قوة إيمانه
|
| AKAPOLO:
Awa ndi:
A- Msilamu yemwe walembeledwa kuti ngati atapeleka ndalama mwakuti basi amasulidwa ukapolo.
B- Kummasula ukapolo msilamu.
C- Msilamu yemwe wagwidwa ukapolo ku nkhondo. |
في الرقاب :
وهم : أ – المكاتب المسلم
ب – إعتاق الرقيق المسلم
ج – الأسير المسلم
|
| OTHINIDWA NDI NGONGOLE:
Awa ndi:
A- Yemwe wagwa mu ngongole chifukwa chofuna kuyanjanitsa anthu omwe asemphana.
B- Yemwe wagwa mu ngongole chifukwa chofuna kuzithandiza pa mavuto ake omwe anamugwera. |
الغارمون :
وهم : أ- غارم لإصلاح ذات البين
ب- غارم لنفسه
|
| YEMWE ALI PA NJIRA YA ALLAH:
Umu mukulowa asilikali a nkhondo ndi kalikonse kamene angasaukile monga zida ndi zina zotero.
|
في سبيل الله :
يشمل الغزاة ومايحتاجون إليه
من سلاح وغيره
|
| WA PAULENDO:
Uyu ndi munthu yemwe wauyamba ulendo ndipo kamba wake wa pa ulendo watha (monga tarasipoti), choncho amapasidwa zokamufikisa kwawo komwe wachokera kapena komwe akulowera. |
ابن السبيل :
وهو المسافر المجتاز الذي قد فرغت نفقته, فيعطى ما يوصله إلى بلده
|