CHICHEWA
اللغة التشيشيوا
MAPEMPHERO A UMRAH
مناسك العمرة
Kuvala nsalu ya ihram.
الإحرام
Kupanga Niyah yolowera mu mapemphero a Umrah
(نيةالدخولفيالنسك)
Malo opangira Niya kapena kuvalira ihram kwa anthu ochokera ku Shami ndi Egypt ndi otchedwa: al-Juhfah mtunda otalika 186 kilometers kuti akafike ku Makkah .
ميقاتأهلالشام
ومصرالجحفة 186 كلم
Anthu ochokera ku Madinah malo awo ndi otchedwa: al-Dhul-Hulayfah, mtunda otalika 420 kilometers.
ميقاتأهلالمدينة
ذوالحليفة 420 كلم
Anthu ochokera ku Iraqi malo awo ndi otchedwa: Dhatu-Iraq, pa mtundu otalika 98 kilometers.
ميقاتأهلالعراق
ذاتعرق 98 كلم
Anthu ochokera ku dera la Najid, malo awo ndi otchedwa: Qarin al-Manāzil, mtunda otalika 99 kilometers.
ميقاتأهلنجد
قرنالمنازل 99 كلم
Ndipo anthu ochokera ku Yemen,malo awo ndi otchedwa: Yalamulam.
ميقاتأهلاليمن
يلملم 99 كلم
Anthu amene akubwera pa ndege, malo awo opangira ihram adzakha omwe ali pafupi ndi iwowo,potengera point iliyonse imene iwo angaoloke m’mambamo,m’malo onse tatchula aja.
يـحـرمالـقادمونعبرالطائرةمنأقربنقطةجـويةعــنــدالـمـرور
بــســماءالميقات
Kuzungulira Kaaba(Twawaf)
الطواف
.
Kuzungulira ma round asanu ndi awiri (7), kuyambila pamene pali mwala WAKUDA kukatheranso pamene pali mwala WAKUDA pomwepo.
سبعة اشواط من الحجر الاسود الى الحجر الاسود
POYAMBILA – POTHERA
بداية – نهاية
KUSWALIRA PAMBUYO PA MALO AMENE AMAIMA IBRAHIM, NGATI ZITATHEKA KUTERO.
الصلاة خلف مقام ابراهيم (امن امكن)
Kenako kukathamanga pakati pa Phiri la al-Aswafā ndi al-Mariwā, utha kumayenda usanafike pa zizindikiro ziwiri za green, ndipo umayenera kuthamanga ukafika pamene pali chizindikiro choyamba cha green cho kukathera pamenenso pali chizindikiro cha green china.Uzithamangako kwambiri, ndipo zimenezi zinaikidwa kwa amuna kuti azithamanga malo amenewa,akazi ayi.
السعيبينالصفاوالمروة
تمشيقبلالعلمينالأخضرينوبينهما
تجريجرياًشديداً
وهوخاصبالرجال
Ma round asanu ndi awiri (7).
ســبعة أشـواط
Kuchokera ku Phiri la al-Aswafā – kukathera ku Phiri la al-Mariwā.
الصفا – المروة
Kumeta mpala kapena kuyepula.
الحلقأوالتقصير
Mpala kapena kuyepula mutu onse,izi ndi za amuna, pamene akazi adzayepula tsitsi lawo ataliphatikiza, pa mulingo wa nsonga ya chala.
الحلقاوالتقصيرللرجل
والمرأةتقصرقدرانملة
Zoletsedwa kwa yemwe walowa mmapempherowa:
محظوراتالإحــرام :
Kuchotsa tsitsi la mmutu kapena pathupi mu njira iliyonseyo.
إزالة الشعر من الرأس والجسد
Kuwenga zikhadabu.
تقليم الأظافر
Kugwiritsa ntchito mafuta onunkhira.
استعمال الطيب
Kumangisa nikkah yako kapena yawina.
عقد النكاح لنفسه أو لغيره
Kukhala malo amodzi ndi mkazi wako.
مباشرة النساء
Kupha zinyama za pamtunda( kupanga ulenje).
قـتـل صـيد الـبـر
Mtundu wa zinthu zoletsedwa kwa amuna okha:
قسم يحرم على الرجال فقط :
Kuvala chovala chosokedwa, ndi ndi chovala chomwe chasokedwe mosiyanitsa ziwalo za thupi, monga panti,talauza kapena malaya, ndiye mukutulukamo chosokedwa ngati siketi.
لبس المخيط وهو ما فصل على الجسمكالثياب أو على عضو من الأعضاء
Kuphimba kumutu ndi chilichonse chomwe chingagundane ndi mutu, monga chipewa,nduwila. Ambulera siikulowa nawo.
تغطية الرأس بملاصق, كالعمامة والطاقية
Mtundu wa zinthu zoletsedwa kwa akazi okha:
قسم يحرم على النساء فقط :
Kuphimba nkhope ndi parada(niqab) kapena burukha,koma ngati pamalopo pali amuna achilendo ndiye atha kuphimba nkhope yake ndi chilichonse.
تغطية الوجه بالنقاب أو البرقع, لكن إذا كانتبحضرة الرجال الأجانب غطت وجهها بخمارها ونحوه
Kuvala ma gulovesi.
لبس القفازين
Zomwe zili zabwino (Sunnah) kwa munthu yemwe akupanga Umrah:
مستحبات العمرة:
Kuwenga zikhadabu, ndi kuchotsa tsitsi limene limafunika kuchotsedwa munthu asanapange niyah ya ihram.
تـقــلـيم الأظــافر و أخــذ الــشــعر الذي يـلزم أخـذه قــبل عـقـد نيـة الإحرام
Kusamba usanavale ihram.
الاغتــســال للإحـرام
kuzinunkhiritsa pathupi usanavale ihram.izi kwa amuna okha akazi ayi.
التطيب في البدن للرجال
Kuvala nsalu ziwiri ya mmusi ndiya muntunda, zonse zoyera,amuna okha okha.
لبس إزار و رداء أبيضين للرجال
Kunena Talibia:(Labbaika Allahumma Labbaika. Labbaika lā sharieka laka Labbaika.Innal-hamda, wannaamata laka wal-mulik.Laa sharieka laka).











