
ZISONYEZO ZA UTUMIKI (CHICHEWA)
(دلائل النبوَّة) و(أعلام النبوَّة) القرآن الكريم تشيشوا ZISONYEZO ZA UTUMIKI (CHICHEWA) QURAN YOLEMEKEZEKA: Adayankhula Yahyah bin Aktham kunena kuti: Māmuun yemwe adali mtsogoleri wa asilamu nthawi imeneyo,adachititsa mkumano wa mtsutso (debate), ndiye kunalowa muyuda wina mchigulu cha anthu omwe anafika ku mtsutso kuja, muyudayu anali atavala bwino, nkhope ikuoneka bwino komanso amamveka kafungo kabwino. Kenako Adayankhula muyuda uja ndipo adayankhula...
ZISONYEZO ZA UTUMIKI (CHICHEWA)
(دلائل النبوَّة) و(أعلام النبوَّة)
القرآن الكريم
تشيشوا
ZISONYEZO ZA UTUMIKI
(CHICHEWA)
QURAN YOLEMEKEZEKA:
Adayankhula Yahyah bin Aktham kunena kuti: Māmuun yemwe adali mtsogoleri wa asilamu nthawi imeneyo,adachititsa mkumano wa mtsutso (debate), ndiye kunalowa muyuda wina mchigulu cha anthu omwe anafika ku mtsutso kuja, muyudayu anali atavala bwino, nkhope ikuoneka bwino komanso amamveka kafungo kabwino.
Kenako Adayankhula muyuda uja ndipo adayankhula bwino kwambiri.
Mkumano wa mtsutso utatha, Māmuun adamuitana muyudayu uja, ndipo anamufunsa kuti: ndiwe muisirayeri( muyuda)?
Muyuda uja anavomera kuti: eya .
Māmuun adamuuza kuti lowa chisilamu, kuti ndikupangire zakuti zakuti, anamulonjeza zompangira zabwino zochuluka ngati angalowe chisilamu.
Muyuda uja adayankha kuti: Ayi ndikhala mu chipembedzo changa ndi chipembedzo cha makolo anga chomwechi. Kenako adanyamuka kumapita.
Chitatha Chaka, Māmuun adachititsanso mkumano wina ndipo kudabweranso muyuda ali Msilamu.
Mu nthawi iyi muyudayu adayankhula(kufotokoza) zokhuzana ndi fiqh komanso hadeeth,ndipo adayankhulanso bwino kwambiri kumbali imeneyi.
Mkumano utatha, Māmuun adamuitana muyuda uja ndipo adamufunsa kunena kuti:kodi si iwe amene tinali naye ulendo watha uja?
Iye adayankha kuti: eya ndi ineyo.
Anamufunsa kuti: ndiye chimene chinakupangitsa kulowa chisilamu ndi chiyani pambuyo pakuti unakana?
Poyankha muyuda adati: vetsera ndipo unene kuti Mulungu ndi wamkulu (Allah Akbar), ndidachoka pa mkumano wako tsiku limene lija, ndipo ndinafuna kuti ndizipange mayeso zipembedzo zimenezi,ine ndimatha kulemba bwino kwambiri. Choncho ndinatenga Chipangano chakale( Torah) ndiye ndinalemba mabuku atatu. Ndinaonjezera zinthu m'menemo ndipo ndinapungulanso zinthu zina. Kenako ndinatenga mabuku aja ndikulowa nawo mu chalichi(church) ndiye anandigula mabuku onse aja ndipo sanakhale ndi nthawi yoti awerenge zomwe zalembedwa m'mabuku aja ndikuona ngati muli zolakwika.
Kenako ndinatenga Chipangano chatsopano(Bible) ndipo ndinalembanso mabuku atatu,ndinaonjezera mmenemo zinthu zoti munalibe komanso kupungula zina zomwe zinalipo. Kenako ndinalowa nawo ma buku aja mmalo opephelera Ayuda ndipo anagulidwa kuchokera kwa ine ma buku onse aja, nawonso awa sanawerenge, m'malo mwake anayamba kuwagwiritsa ntchito.
Kenako ndinatenga Quran ndipo ndinalembanso mabuku atatu ndinapita nawo kwa opanga print/copy iwo anati sitingalandile mpaka titawerenga kaye ndikuona zomwe zili mkatimo ngati zikugwirizana ndi Quran yathu, atawerenga anazitulukila zolakwika zomwe zinali mmenemo monga kuonjezera ndi kupungula , adaima ndi kwaotcha mabuku onse aja , ndipo anatsala pang'ono kundipha.
Kuchokera pamenepo ndinadziwa kuti buku ili la Quran ndi losungidwa ndipo lotetezedwa ndi Allah.
Chimenechi ndicho chifukwa chakulowa kwanga chisilamu.
File | Action |
---|---|
photo_٢٠٢٥-٠٤-٢٥_٢٠-٣٢-٤٧.jpg | Download |

ZISONYEZO ZA UTUMIKI (CHICHEWA)
Scan QR Code | Use a QR Code Scanner to fast download directly to your mobile device